Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 406

Paphata pa Chichewa Zothyakuka: Zomveka komanso zanzeru. Chitsanzo: Amakamba zothyakuka. Zotoleza: Zopeza movutikira, zochepa. Chitsanzo: Ife timadya zakudya zotoleza. Zotsina zam’moyo: Mavuto. Chitsanzo: Munthu umakhala ndi nzeru ukamakumana ndi zotsina zam’moyo. Zotsinatsina zam’thupi: Matenda, timatenda ting’onoting’ono. Chitsanzo: Tili bwino, zotsinatsina zam’thupizi osalephera. Zotsirika: Zotetezedwa ndi mankhwala kuti wina asabe. Chitsanzo: Waba chimanga chotsirika. Zoumitsa thupi: Zochititsa mantha Chitsanzo: Zimene zachitika ndi zoumitsa thupi. Zovala zapadama: Zovala zoyenera pagulu. Chitsanzo: Ndi ochepa amene masiku ano akumavala zovala zapadama. Zovala zoononga ulusi: Zovala zazikulu. Chitsanzo: Anyamata onse omwe amavala zovala zoononga ulusi n’ngofunika kukawaika kumiziyamu! Zovala zovalira therere: Zovala zothika kwambiri. Chitsanzo: Anyamata ndi atsikana a masiku ano akumavala zovala zovalira therere. Zovuta (zavuta): Maliro. Chitsanzo: (1) Pakhomo pakachitika zovuta, mumafunika kaye muuze amfumu musanayambe kulira. (2) Zavutatu uku! Zowerengeka: Zochepa. Chitsanzo: Pamalo paja patsala zinthu zowerengeka. Zozizira: Zosagwira mtima kwenikweni, zopanda nzeru, zosathandiza, zopanda mphamvu. Chitsanzo: Nthawi zonse nkhani zimene amakamba 405