Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 405
Paphata pa Chichewa
zosamveka, munthu ungabwereke bwanji ndalama
n’cholinga choti ukabwereketse wina.
Zosaneneka:
(a) Zambirimbiri.
Chitsanzo: Ali pamavuto osaneneka.
(b) Zovuta kutchula.
Chitsanzo: Zimene ndaona ndi zosaneneka.
Zosapsa:
(a) Zosatsimikizirika.
Chitsanzo: Ndimadana ndi anthu amene amati akamva
nkhani zosapsa n’kuyamba kuuza ena.
(b) Zosagwira mtima, zosamveka bwino, zosathyakuka.
Chitsanzo: Nkhani imene mwalembayi ndi yosapsa.
Zosawa: Zokhala ndi madzi ambiri, m’madera ena
amagwiritsa ntchito mawuwa akamanena za zinthu
zowawa.
Chitsanzo: Chinagwa chosawa sichikoma.
Zosawerengeka: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Ali ndi masapota osawerengeka.
Zosayenera:
(a) Zinthu zoipa,
Chitsanzo: Zimene akuchitazi ndi zosayenera.
(b) Chiwerewere.
Chitsanzo: Ukagwidwa ukuchita zosayenera, mbiri yako
imada.
Zothasamala: Zafulati.
Chitsanzo: Mukatenge zothasamala zokhazokha.
Zothetsa mankhalu: Zovutitsitsa, zosatheka.
Chitsanzo: Mayeso ake anali ovuta mothetsa mankhalu.
Zothinana: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Kumunda kwawo kuli nthochi zothinana.
404