Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 376
Paphata pa Chichewa
(2) Amuwamba ndi chitsulo chamoto.
(b) Chinthu chofala, chinthu chomwe si chapamwamba,
munthu yemwe alibe udindo ulionse, munthu wosauka.
Chitsanzo: (1) Kuno sikulowa anthu wamba. (2)
Sindingagule njinga za wamba.
Wamfupimapazi: Mkazi.
Chitsanzo: Wachita zimenezi ayenera ndi wamfupimapazi.
Wamtalizala: Munthu wakuba.
Chitsanzo: Chenjerani naye munthuyu, ndi wamtalizala.
Wamutu wofuna jeke: Wamkulu mutu.
Chitsanzo: Ndani anakuuza kuti anthu amitu yofuna jeke
amakhala anzeru?
Wamutu woipa: Munthu yemwe amalota maloto oipa
kwambiri.
Chitsanzo: Ndikaona zinthu zochititsa mantha sindigona.
Mutu wanga ndi woipa.
Wamutu wophikika: Wosokonekera, wopanda nzeru.
Chitsanzo: Ana awo ndi a mitu yophikika.
Wamutu wosukusa: Wopanda nzeru.
Chitsanzo: Asabwere kuno amene uja, sitifuna anthu a
mitu yosukusa.
Wamvulazakale: Munthu wakalamba.
Chitsanzo: Amvulazakale akumaganiziridwa kuti ndi afiti.
Wamwera zake: Waledzera kwambiri.
Chitsanzo: Ndakumana naye ali dzandidzandi. Zikuoneka
kuti wamwera zake.
Wandikama: Wandidyera ndalama zanga zonse,
akungofuna ndimupatse ndalama.
Chitsanzo: Akabwera pakhomo pano n’kufunsa dzina
langa, ndimachita kudziwiratu kuti akufuna andikame.
Wanditengamo: Wandipsetsa mtima.
Chitsanzo: Mnyamata amene uja wanditengamo. Zoona
kufupika kumene kuja angandiuze kuti amandifuna?
375