Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 375
Paphata pa Chichewa
(2) Mtsikana amene uja ndi wam’kamwa.
Wam’leka wapamwala: Kusiya munthu chifukwa ndi
wovuta kapena tambwali.
Chitsanzo: Atsikana ena amavuta kuwafunsira moti
anyamata ambiri amaona kuti ndi bwino kungom’leka
wapamwala.
Wam’lomo: Wolongolola.
Chitsanzo: Mkazi wake ndi wam’lomo.
Wam’mutu:
(a) Wamisala.
Chitsanzo: Mkazi wake uja ndi wam’mutu.
(b) Wovuta, wosaganiza bwino.
Chitsanzo: (1) Mwanayu ndi wam’mutu. (2) Mayi aja ndi
am’mutu.
Wamabodza: Wokonda kunena zabodza.
Chitsanzo: Kamwana aka ndi kamabodza.
Wamagwiragwira: Wachiwerewere.
Chitsanzo: Mnyamata ameneyu ndi wamagwiragwira.
Wamanjaaatali: Munthu wolemera.
Chitsanzo: Amene uja ndi wamanjaaatali.
Wamanjalende: Waulesi.
Chitsanzo: Ndani angakwatire mkazi wamanjalende.
Wamasiye: Munthu yemwe bambo, mayi, mkazi kapena
mwamuna wake anamwalira.
Chitsanzo: Mmene wakuliramu ungamanene kuti ndiwe
mwana wamasiye?
Wamba:
(a) Kuwaula nyama kuti ichoke ubweya kapena iume
pang’ono, kuumitsa nsomba ndi ndiwo zina, kuwaula
chinthu.
Chitsanzo: (1) Yambani mwawamba nkhukuyi.
374