Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 373
Paphata pa Chichewa
Wachiyera: Nzungu.
Chitsanzo: Kukubwera munthu wachiyera.
Wada (wachita mdima): Wachita manyazi.
Chitsanzo: (1) Nkhope yake yachita mdima. (2) Mnyamata
uja wada.
Waduka lende: Kukumana ndi mavuto.
Munthu ukakhala palende lendeyo n’kuduka umagwa
pansi.
Chitsanzo: Mkaziyu azunzika koopsa chifukwa anaduka
lende, mwamuna wake atangomwalira.
Wadya ndalama: Wawononga ndalama.
Chitsanzo: Munthu ameneyu wadya ndalama zanga.
Wadyapo: Mawu amene anthu amanena mwachipongwe
wina akapweteka. Mawuwa amatanthauza wachita bwino
wapweteka.
Chitsanzo: “Ndinakuuza kuti uziyang’ana pansi.
Wadyapo!”
Wadyera pamwamba: Wadziwika.
Chitsanzo: Amayenda m’mbali, lerotu wadziwika.
Amugwira akudyera pamwamba.
Wadyera zake (wamwera zake): Waledzera kwambiri.
Chitsanzo: Ndakumana naye ali dzandidzandi. Zikuoneka
kuti wadyera zake.
Wadzitho: Wamphamvu.
Chitsanzo: (1) Akufuna anyamata adzitho. (2)
Mnyamatayu ndi wadzitho.
Wafawafa: Kulimbana kwambiri pampikisano.
Chitsanzo: Masewerawa afika mundime ya wafawafa.
Wafodya: Wopanda nzeru.
Chitsanzo: Akulu amene aja ndi afodya, asadzabwerenso
kuno!
372