Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 372
Paphata pa Chichewa
Wa Adamu: Kuyenda wapansi.
Chitsanzo: Ngakhale sukulu yawo ili kutali, mnyamatayo
amayenda wa Adamu.
Wachabe:
(a) Munthu woipa.
Chitsanzo: Munthu amene uja ndi wachabe.
(b) Katswiri.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wachabe pankhani ya mpira.
(c) Kubwera opanda kanthu.
Chitsanzo: Angoyenda wachabe.
Wachabechabe (chachabechabe): Wopanda ntchito,
wosafunika, chinthu chakutha.
Chitsanzo: (1) Wantchitoyu ndi wachabechabe. (2)
Andigulitsa wailesi yachabechabe.
Wachamba:
(a) Wopanda nzeru.
Chitsanzo: Ndiwe Wachamba eti?
(b) Munthu amene amasuta chamba.
Chitsanzo: Panadutsa bambo wachamba uja.
Wachepa: Ndi mwana.
Chitsanzo: Wachepa, sungalimbane ndi ine.
Wachikulire:
(a) Munthu wokalamba.
Chitsanzo: Bambo awo ndi achikulire.
(b) Bwana, wolemekezeka.
Chitsanzo: (1) Amene uja ndi wachikulire pakampanipa.
(2) Ameneyu ndi wachikulire pa nkhani zoimbaimbazi.
Wachimasomaso: Munthu wokonda amuna kapena
akazi, hule.
Chitsanzo: (1) M’nyumba iyi mumakhala azimayi
achimasomaso. (2) Ngati Katakwe ali munthudi, wayenera
kukhala wachimasomaso.
371