Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 336

Paphata pa Chichewa mwana ankawasambitsira mu nkhate n’chifukwa chake amayenda ndi tsoka. Chitsanzo: Lerotu ndiye mwasambira munkhate. Sambitsa chokweza: Kuchenjeretsa, kulanga munthu kapena kumuwonongera chuma. Chitsanzo: (1) Ngofunika kumusambitsa chokweza. (2) Osewera mpira a dziko lino asambitsidwa chokweza ndi osewera a ku Zimbabwe. Sambula: Nyoza kotheratu, kunena munthu chipongwe. Chitsanzo: (1) Mayi amene aja amawasambula amuna awo. Koma m’mawa kukacha, amanyamuka n’kuka- wasiyira madzi kubafa. (2) Koma ndiye mwandisambulatu! Sambwadza: Kukalipira, kulalatira munthu. Chitsanzo: Abwana ake amusambwadza. Samezamate: Munthu yemwe akayamba kuyankhula sasiya, wolongolola. Chitsanzo: Mkazi wake uja ndi samezamate. Samisoni: Munthu wamphamvu. Chitsanzo: Anzathu aja anakwatiwa ndi Samisoni. Samuka: Kuchokapo kupita kwina. Chitsanzo: Ndikawaona akubwera ndingosamukapo! Samvamkunkhu: Munthu wopirira amene sathawa nga- khale amenyedwe. Chitsanzo: Anyoni ndi samvamkunkhu. Samvamtsonyo: Munthu amene samasamala ngakhale anzake azimunyoza. Chitsanzo: Anasiyani ndi samvamtsonyo, umati ukawanena, mawa amabwera kwanu kudzapempha mchere. Sanatalikire: Sanapite kutali. Chitsanzo: Adikireni, sanatalikire. 335