Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 335

Paphata pa Chichewa Sagwira pakamwa: Munthu wosabisa kanthu kapena wosasunga chinsinsi. Chitsanzo: Amene ajatu satha kugwira pakamwa. Sainunkha: Sadya nawo. Chitsanzo: Akapitiriza kuchita mwano sainunkha lero. Saka: (a) Chiguduli, thumba. Chitsanzo: Longedzani zinthuzi musaka. (b) Kufufuza chinachake. Chitsanzo: Apita kosaka nyama. Samba nane pakumwa: Kukhaulitsa, kukuonetsa zimene sunaonepo chibadwire. Chitsanzo: Akuyerekedwa kwambiri, asamba nane pa- kumwa. Samba pakamwa: Kukometsa mawu. Chitsanzo: Anthu ena akaona kuti mwana wawo wapalamula amasamba pakamwa, koma akakhala wa ena ndiye matukutuku. Samba pakumwa: Palamula. Chitsanzo: Amene uja amuthamangitsa pamudzi pano. Wasamba pakumwa. Samba: Matenda amene akazi amadwala mwezi ndi mwezi. Chitsanzo: Mwina ndaima, ndinasiya kusamba miyezi iwiri yapitayo. Sambira m’nkhali: Chita mwayi. Chitsanzo: (1) Inuyo ndi amene mwachititsa kuti tisambire m’nkhali lero. (2) Munakapanda kutichitira zimenezi sitikanasambira m’nkhali lero. Sambira munkhate: Chita tsoka. Munthu wina anapita kunyumba kwa ena n’kukawapeza akumaliza kumene kudya. Anthuwo anamuuza kuti ali 334