Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 312
Paphata pa Chichewa
Odalirika: Munthu amene sangakugwiritse mwala.
Chitsanzo: Uyu ndi munthu wodalilika.
Okanika: Osamva, osathandizika.
Chitsanzo: Anthu ake ndi okanika, kuwalangiza samva.
Okhupuka: Olemera.
Chitsanzo: Banja lawo lonse ndi lokhupuka.
Okungana: Ovuta.
Chitsanzo: Ndikukumana ndi mavuto okungana.
Olimba: Opirira, amphamvu.
Chitsanzo: (1) Mwana uyu ndi wolimba. (2) Anthu a
m’dera limeneli ndi olimba.
Oloka: Kumaliza kusamba komwe ndi matenda amene
akazi amadwala mwezi ndi mwezi.
Chitsanzo: Ndinaoloka masiku awiri apitawo.
Olokera pa kangaude: Kuchita mwayi utakumana ndi
mavuto oti sukanapulumuka.
Chitsanzo: Anangotsala pang’ono kundigwira moti
ndangoolokera pakangaude.
Olotsa azungu: Kazinga chimanga.
Chitsanzo: Uzani alendowa azipita kuti ife tiolotse azungu.
Olowa: Kufewa.
Chitsanzo: Mpunga unaviika uja wawolowa.
Omba bumi: Peza palibe.
Chitsanzo: Anandiuza kuti chimanga chilipo, koma
nditafika ndinaomba bumi chifukwa ndinachipeza
chitatha.
Omba khoma: Kupita kwina n’kusapeza zimene ukufuna.
Chitsanzo: Ndimaganiza kuti ndikawapeza ali pakhomo,
koma ndaomba khoma.
Omba mfuti: Kuchita choipa.
Chitsanzo: Mwana wa a Nasiyani waomba mfuti.
311