Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 289
Paphata pa Chichewa
(b) Kupusa.
Chitsanzo: Munthu wake amangoti ndungundu.
Nduu: Mulu, kuunjikana.
Chitsanzo: Ndinapeza zovala zakuda zili nduu!
Ndwii: Mmene munthu amaonekera akakhumudwa
kapena akamasowa chochita.
Chitsanzo: Ndinawapeza ali ndwii pakhonde.
Neng’a: Kukhala pampando kapena pabedi kwinaku
ukumva bwino.
Chitsanzo: Ndinamupeza ali neng’a, pampando.
Ng’amba chipika: Waza nkhuni.
Chitsanzo: Anyamata amphamvu apite kuseriku kuti
akang’ambe zipika.
Ng’amba khofi: Kupatsa munthu wina khofi
mwamphamvu.
Chitsanzo: Mayiwa awang’amba khofi amuna awo.
Ng’amba kukamwa: Kuyankhula kwambiri, kuyankhula
kapena kulira mokweza kwambiri.
Chitsanzo: (1) Ukufuna ndichite kung’amba kukamwa
kuti umve! (2) Kodi ndi ndani akung’amba kukamwayo?
Ng’amba:
(a) Chilala
Chitsanzo: Amene atapulumuke ng’amba imeneyi ndi
mwamuna.
(b) Kuona zoopsa.
Chitsanzo: Amachita masewera ndi njuchi, ndiye
zamuonetsa ng’amba.
Ng’anjo: Moto waukulu.
Chitsanzo: Sitimakazinga chimanga ndi ng’anjo, chimatha
ndi kupserera.
Ng’oma: Munthu wotchuka kapena wodziwika kwambiri.
Mawuwa anayamba chifukwa ng’omba imamveka patali.
288