Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 288
Paphata pa Chichewa
Ndondocha: Munthu wamimba youma ngati mpira, mun-
thu wodya kwambiri. Mawuwa anayamba kuchokera ku
zikhulupiriro zoti afiti amatha kusunga tianthu ta mimba
zikuluzikulu kuti aziwagwirira ntchito kapena kuwalimira
m’munda.
Chitsanzo: (1) Mwana wanuyu amadya ngati ndondocha.
(2) Ana awo onse ndi ndondocha.
Ndondola: Yenda mofulumira ngati mbalame.
Chitsanzo: Akundondola kulowera uku.
Ndondoli: Malovu omwe akuyoyoka kapena kuchucha
kuchokera pakamwa.
Chitsanzo: Ngakhale utakhala kuti umagwetsa ndondoli
sindingakusiye.
Ndondomeko: Dongosolo lake, mwatsatanetsatane.
Chitsanzo: Ukamachita zimenezi umafunika kutsatira
ndondomeko yake.
Nduke: Akazi okongola.
Chitsanzo: Mtauni mumakhala nduke zosalitsa tulo.
Ndulu: Chinthu chowawa chimene chimapezeka mkati
mwa nkhuku komanso zinthu zina. Anganenedwe ponena
kuti chinachake ndi chowawa kwambiri.
Chitsanzo: Mankhwalawa ndi ndulu.
Ndundu: Anthu ovuta.
Chitsanzo: Ndundu zachoka, tsopano timasuke.
Ndundundu (ndu): Kudzadziratu, zambiri.
Chitsanzo: Mchenga wangoti ndundundu pakhonde.
Ndundundu: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Tinapeza chimanga chili ndundundu m’nyum-
bamo.
Ndungundu:
(a) Kungokhala ndwii, kukwiya.
Chitsanzo: Kumasekako, osamangokhala ndungundu!
287