Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 277
Paphata pa Chichewa
anawauza mwakutimwakuti.
Mwambo: Zochitika. Nthawi zina mawuwa amagwiritsid-
wa ntchito mwachining’a ponena za kudya chakudya.
Tanthauzo lake lenileni ndi zinthu zimene mumazichita
chifukwa choti munazolowera kapena potsatira zimene zi-
nayamba kale kuchitika.
Chitsanzo: Mwambotu wayambika m’nyumbamu!
Mwamuna mnzako mpachulu: Osamanyoza mwamuna
mnzako usakudziwa mphamvu zake chifukwa akhoza ku-
kubwanyula.
Chitsanzo: Akundiderera? Sakudziwa kuti mwamuna
mnzako mpachulu?
Mwamvu: Chilimwe.
Chitsanzo: Amakonda kupita kutauni m’nyengo ya
mwamvu.
Mwamwambo: Kungochita chifukwa choti unazolowera
kapena ukuyenera kuchita zimenezo basi.
Chitsanzo: Ana amene amalephera mayeso amangopita
kusukulu mwamwambo basi.
Mwana amalira ndi mkodzo wake womwe: Kuchita zin-
thu chifukwa chosaganiza bwino kenako n’kumasintha
ukudandaula.
Chitsanzo: Si paja tinagwirizana kuti ukagwira mtaji usa-
masiye, ndiye pano ukubwezanso mawu ako? Ndithudi
mwana amalira ndi mkodzo wake womwe.
Mwana wachisamba: Mwana woyamba kubadwa.
Chitsanzo: Uyu ndi amene anaperekeza, tinakumana naye
panjira uja ndiye chisamba.
Mwana wamatumbo walira: Njala.
Chitsanzo: Mwana wamatumbo walira, tiphike nsima.
Mwana wapatchire (wapathengo): Mwana wobadwira ku-
chibwenzi kapena amene anabadwa makolo ake asanak-
watirane, mwana yemwe wabadwa kunja kwa ukwati.
276