Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 276
Paphata pa Chichewa
ndikuwayang’anira azichita zinthu mwachisawawa.
Mwado: Panti, kabudula wamkati.
Chitsanzo: Mwana wawoyu savala mwado.
Mwadza mwatha: Mwabwera basi palibenso chimene
mungachite.
Chitsanzo: Mwadza mwatha, ingolimbani mtima.
Mwafuli: Ambulela.
Chitsanzo: Ndimakumbukira kutenga mwafuli mvula
ikamagwa.
Mwagwa nayo: Mwalephera.
Chitsanzo: Ngati mumaganiza kuti mupambana, mwagwa
nayo!
Mwagwira ntchito: Mwandithandiza.
Chitsanzo: Pamenepatu mwagwira ntchito, lero tidya
chifukwa cha inu.
Mwakachetechete: Mosaonetsera, mwachinsinsi,
mosapanga phokoso.
Chitsanzo: (1) Anangobwera mwakachetechete
n’kuwapezerera akuwanena. (2) Muzichita zinthu
mwakachetechete.
Mwakachetechete: Mosayankhula.
Chitsanzo: (1) Muzingolemba mwakachetechete. (2)
Analowa mwakachetechete.
Mwakathithi: Mopanikiza, mosasiya, zambiri.
Chitsanzo: (1) Chaka chino mvula yabwera mwakathithi.
(2) Chimangachi munachidzala mwakathithi.
Mwakulamwatha: Mawuwa amanenedwa pouza munthu
wina kuti aziona.
Chitsanzo: Mwana amene uja wakulawatha.
Mwakutimwakuti: Mawuwa amanenedwa ngati
munthuyo sakufuna kunena mawu enieni.
Chitsanzo: Nditakumana nawo anayamba kunena kuti
275