Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 257
Paphata pa Chichewa
Mkazi wotchipa:
(a) Mkazi wosalira zambiri.
Chitsanzo: Sindifuna mkazi wofuna zambiri, ndisakasaka
wotchipa.
(b) Mkazi wachimasomaso.
Chitsanzo: Mtaunimu muli akazi ambiri otchipa.
Mkhalakale:
(a) Nkhalamba, munthu wokalamba.
Chitsanzo: (1) Chifukwa choti nkhalakale zambiri zinatha
mano m’kamwa, umafunika kumazisinjira chigodo kapena
m’bwibwi. (2) Ukafuna malangizo othandiza, umafunika
kufunsa nkhalakale.
(b) Munthu amene wakhala nthawi yaitali pamalo enaake
Chitsanzo: Musanayambe kugwira ntchitoyi, funsani kaye
ankhalakale.
Mkokemkoke: Kukanganirana, kulimbana.
Chitsanzo: Lero kwa ADMARC kunali mkokemkoke.
Mkoko: Zonse pamodzi monga mmene imakhalira nthochi
isanadulidwe m’mapava.
Chitsanzo: Wanyamula mkoko wanthochi.
Mkokomo:
(a) Phokoso la kuyenda kwa chinthu.
Chitsanzo: Ndikumva mkokomo wa ndege.
(b) Mwaphuma, mwaphokoso.
Chitsanzo: (1) Anafika pamowapo mwamkokomo, ngakhale
analibe chilichonse. (2) Amayenda mwamkokomo.
Mkolamawu: Wailesi.
Chitsanzo: Wailesi ikungobwera kumene anthu
ankaitchula kuti mkolamawu.
Mkondwa:
(a) Chisangalalo chachikulu chosafuna kusiya.
Chitsanzo: Mukadzaiona mbuzi ili pa mkondwa, muzadzi-
we kuti amalonda ayandikira.
256