Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 256
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Sindingapite kukawaona popanda mituka.
Mizu yakachere: Kukumana, kupangana zinazake.
Chitsanzo: Amaoneka kuti sagwirizana, koma ndi mizu
yakachere.
Mjedo (mijedo): Kunena miseche, kunena munthu wina
kuseri.
Chitsanzo: Mayiwa ndi a mjedo (mijedo).
Mkacha: Mawu amenewa ndi dzina la ukonde wamaso
aang’ono womwe umakokolola nsomba iliyonse ndi
zazing’ono zomwe. Mawuwa amanenedwa ngati munthu
watenga matenda kapena wagwera m’mavuto enaake
chifukwa cha zochita zake.
Chitsanzo: Nawonso anakokololedwa ndi mkacha wa ka-
chilombo.
Mkamwini wankhanga: Mwamuna wolima kwambiri.
Chitsanzo: Pakhomo pano timafuna akamwini ankhanga.
Mkangaziwisi: Munthu wosaopa kugwira ntchito
ngakhale itakhala yovuta.
Chitsanzo: Anthu amene amagwira ntchito kumotchale
amakhala a mkangaziwisi. Ena amadyera nsima
m’motchale momwemo.
Mkango: Munthu wovuta kapena wankhanza.
Chitsanzo: Mayi aja anakwatiwa ndi mkango. Amangow-
amenya tsiku ndi tsiku.
Mkazi wamalonda: Hule, mkazi wachimasomaso, mkazi
woyendayenda, mkazi wokonda amuna.
Chitsanzo: Mkazi wamalonda anabwera kwawo ndipo
amanena kuti akufuna zake.
Mkazi wapambali: Mkazi wachiwiri, mkazi wachibwenzi.
Chitsanzo: Amuna awo ali ndi mkazi wapambali.
255