Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 171

Paphata pa Chichewa Kunyowa: Kuchita manyazi. Chitsanzo: (1) Koma ndiye mwanyowatu, mpaka kukalipidwa pamaso pa akazi anu? (2) Mnyamata uja ndiye wanyowa, zoona kumuyendetsa osavala. Kunyowa: Kuchita manyazi. Chitsanzo: Nditayankhula zimenezo ndinanyowa. Kunyozeka: Kuchita manyazi, kupusa. Chitsanzo: (1) Koma ndiye anyozekatu mayiwa, kugwa pagulu ngati pano! (2) Mwanayo anaona bambo ake akun- yozeka. Kunyozololoka: Kuonda chifukwa cha matenda kapena kusowa chakudya m’thupi. Chitsanzo: Mwanayu mukamapanda kumudyetsa anyozo- loloka. Kunyumwa: Kudabwa. Chitsanzo: Ndainyumwa, n’chifukwa chiyani akundiuza kuti ndipite ndekha. Kunyumwitsa: Kuopseza wina. Chitsanzo: Anyamata aja amandinyumwitsa. Kunzi: Mphongo. Chitsanzo: Ntchito zina zimafuna kunzi. Kuolobza: Kufewetsa. Chitsanzo: Mate amaolobza shuga kuti akome kwambiri. Kuoloka moto: Kugonana. Chitsanzo: Anawapezerera akuoloka moto. Kuolowa manja: Kukhala munthu wopatsa. Chitsanzo: Ukakhala woolowa manja, anthu amakuzolow- era. 170