Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 170

Paphata pa Chichewa kunyindirira liwiro. Kunyinduka: Kuphwanyika, kubwanyuka. Chitsanzo: Nkhumba idagwa ndi chipumi mphuno yake n’kunyinduka. Kunyindula: (a) Mawuwa anganenedwe mwachipongwe ponena za munthu amene akuyankhula. Chitsanzo: Sindifuna kuti munthu amene ndikumuthandiza azinyindulanso pakamwa. (b) Kuphwanyika pakamwa, kapena kupanyansitsa. Chitsanzo: Nkhumba inanyinduka kamwa itagwa mumtengo chifukwa cha dyera. (c) Mawu onyoza kwambiri onena munthu akamadya potengera mmene pakamwa pake pakuonekera makamaka pokudya. Chitsanzo: Tazingonyindulani nsimayi apa! Kunyinyirika: Kusafuna kuchita zinazake, kukana kuchita chinachake, mwano. Chitsanzo: Ndikamutuma amakonda kunyinyirika. Kunyong’olera: Kuchotsa zomwe zatsakamira m’kamwa ukamaliza kudya. Ena amachotsa ndi lilime kapena kuyendetsayendetsa minofu ya m’kamwa. Chitsanzo: Amene akunyong’olera wadya kale. Kunyong’onyeka: Kusowa mtendere, kusaona bwino. Chitsanzo: Ndikakhala pakhomo ndimanyong’onyeka. Kunyonyomala: Kunjuta posonyeza ulemu. Chitsanzo: Mnyamata amafunika azinyonyomala pamaso pa akulu. 169