Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 161

Paphata pa Chichewa (c) Kuuza munthu kuti asamangike, azichita zinthu mopanda mantha. Chitsanzo: Takulandirani! Khalani omasuka, kuno ndi kwanu. (d) Kuyankhula mosabisa mawu. Chitsanzo: Amati atani, lero lokha ndiye ndawamasula! Kumasula: Kuuza munthu chilungamo. Chitsanzo: Lero lokha ndiye ndikumasulani! Kumata phula m’maso: Kunamiza kapena kupusitsa munthu. Chitsanzo: (1) Anandimata phula m’maso kuti amakonza mafoni, nditangomupatsa, anangolowa m’dzombe n’kuzimiririka. (2) Mnyamatayo anawamata anthu onse phula m’maso, powanamiza kuti wachokera kujoni pomwe ndi wapamtundapa. Kumbiyazodooka: Kumanda. Chitsanzo: Masiku ano mitengo yatsala kumbiyazodooka kokha. Kumbuyo kulibe maso: Zakumbuyo sizidziwika. Chitsanzo: Sindingalole kuti ndizidwala m’mimba chifukwa cha zimene zinachitika chaka chatha. Kumbuyo kulibe maso! Kumbwandira: Kugwira. Chitsanzo: Amumbwandira akuthyola mzimbe m’munda wa eni. Kumeneko ndiye kukhala: Mawuwa amanenedwa pothokoza wina kutanthauza kuti zimene munthuyo wachita ndi zoyenera kapena zabwino. 160