Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 160

Paphata pa Chichewa Mpofunika timumangire mpanda. Kumasano: Kumanda. Chitsanzo: Anamupeza akuthyola mango kumasano. Kumaso: Maliseche. Chitsanzo: Analira koopsa atamumenya kumaso. Kumasuka: (a) Kuchita zinthu mosamangika. Chitsanzo: (1) Muzichita zinthu momasuka. (2) Khalani omasuka kufunsa funso lililonse. (b) Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene akuuza anzake kuti akhoza kunyamuka. Chitsanzo: Tsopano mukhoza kumasuka. (c) Kupita kuchimbudzi, kudzithandiza, kubiba. Chitsanzo: Zitawavuta, analowa patchire kuti akamasuke. (d) Kusiyana nawo mavuto. Chitsanzo: Ndipite ku Jubeki kuti ndimasuke ku mavutowa. Kumasuka: (a) Kuchita zinthu mopanda manyazi. Chitsanzo: Akunjira, khalani omasuka. (b) Kubiba, kudzithandiza. Chitsanzo: Apita kokamasuka. Kumasula munthu: (a) Kutulutsa munthu amene anamangidwa kundende, kuchotsa zingwe zomwe munamumangira munthu. Chitsanzo: Munthu anamangidwa uja wamasulidwa. (b) Kuuza munthu kuti adzipita. Chitsanzo: Nonse amene mwamaliza takumasulani. 159