Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 16

Paphata pa Chichewa Banyira (basela): Zinthu zongowonjezera, pulaizi. Chitsanzo: Atigula zambiri, apatseniko banyira (basela). Basopo! Mawu amene anthu ena amanena akamafuna kuchenjeza munthu kuti asamale chifukwa akhoza kumumenya kapena kumuchita zoopsa. Chitsanzo: Basopo! Ukachitanso zimenezi ndikuswa. Batiza: Kuyamba kuchita nawo zinazake zomwe poyamba sunkachita kapena kuchititsa munthu wina kuyamba kuchita zimene sankachita poyamba. Mawuwa amatanthauzanso mwambo womwe achipembedzo amachita pomiza munthu m’madzi kapena kumuwaza madzi monga chizindikiro choti munthuyo walowa tchalitchi chawo. Chitsanzo: Amakonda mowa ndi awa, koma anawabatiza anzawowo. Beba: (a) Kusangalatsa kapena kukoma. Chitsanzo: (1) Maunguwa akubeba. (2) Masewerawa akubeba. (b) Kufika pachimake. Chitsanzo: Chibwenzi chawo chafika pobeba. (c) Kukolera. Chitsanzo: Kupizani motowo kuti ubebe. Bembelezi: Munthu wamawu aakulu (abesi), Chilombo chomwe chimasokosera kwambiri (chilombochi chimakhala chakuda ndipo chimakonda kuboola mitengo kapena matabwa.) Chitsanzo: Akamayankhula amangokhala ngati bembelezi. 15