Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 15

Paphata pa Chichewa Babada wapansi: Kuyenda wapansi. Chitsanzo: Chifukwa choti analibe ndalama, anangoyamba kuubabada wapansi. Baka: Kudya. Chitsanzo: Ndinawapeza akubaka nsima. Bakayawo: Mawu amanenedwa pofotokoza za munthu kapena chinthu chimene chatuwa mbuu. Nsomba ya bakayawo imakonda kupezeka m’nyanja zamchere ndiye zikamagulitsidwa zimakhala zotuwa mbuu chifukwa cha mcherewo. Chitsanzo: Anthu amene asamba osadzola mafuta, amangokhala ngati bakayawo. Balamanthu (fwanthu): Kunyamuka mwadzidzidzi. Chitsanzo: Atazindikira kuti kumbuyo kwake kukuyenda njoka, anangoti balamanthu! (fwanthu). Bamantha: Menya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Anamubamantha anzake. Bambo akunyumba: Mawuwa amanenedwa ndi mzimayi ponena za mwamuna wake kapena akamalozera ena mwamuna wake. Chitsanzo: Amenewa ndiye bambo a kunyumba. Bangula: Lira mokweza. Chitsanzo: Ndinamupeza akubangula. Banja la kholo limodzi: Mayi kapena bambo amene amalera yekha ana. Chitsanzo: Mabanja a kholo limozi akuchuluka. 14