Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 154
Paphata pa Chichewa
Kulingana: Kufanana.
Chitsanzo: Ntchitoyi si yolingana ndi msinkhu wake.
Kulingitsa: Kuyesetsa.
Chitsanzo: Ndikupita kuchipatala kukalingitsa magazi.
Kulipweteka khasu: Kulima kwambiri.
Chitsanzo: Akamwini omwe amalipweteka khasu ama-
kondedwa pamudzi.
Kulipweteka thobwa (kapena chakudya china): Kumwa
thobwa lambiri.
Chitsanzo: Tinapeza ataphika thobwa moti tinalipweteka
kwabasi. (2) Njala inatipha moti tinaipweteka nsima.
Kulirira kuutsi: Kulira mobisa misozi. Mawuwa anabwera
kuchokera kukankhani ka Kalulu. Makolo ake atafa ana-
kalowa m’khitchini n’kumakalira. Anachita zimenezi kuti
anzake aziganiza kuti akulira chifukwa cha utsi osati chi-
soni.
Chitsanzo: Anzanu aja akulirira kuutsi.
Kuliyatsa liwiro: Kuthawa, kuthamanga kwambiri.
Chitsanzo: Zikavuta umafunika kungoliyatsa liwiro.
Kuliza mingoli: Kuchita mkonono.
Chitsanzo: Anthu amene amati akagona n’kumaliza min-
goli sangagone patchire, afisi akhoza kuwatola.
Kulobodoka (lobodolobodo): Kupanda mphamvu,
kufooka.
Chitsanzo: (1) Munthu wake amayenda molobodoka. (2)
Bamboyo ndi wolobodoka. (3) Ndinakumana nawo ali lo-
bodolobodo.
153