Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 153

Paphata pa Chichewa Kulibe manda a mbeta: Mawuwa amatanthauza kuti n’zotheka kukhala wekha wosakwatira kapena kukwa- tiwa. Chitsanzo: Sindidandaula kukhala ndekha, munamva zoti kuli manda a mbeta! Kulichete: Kumanda. Chitsanzo: Mukamva zii ndiye kuti ndatsikira kulichete. Kulifwafwantha bodza: Kunama kopanda nako manyazi. Chitsanzo: Atawanamiza makolo athu oyambirira, Satana analifwafwanthanso bodza lina. Ananena kuti kufa simudzafa. Kulikumba liwiro: Kuthamanga kwambiri. Chitsanzo: Ukaona kuti pathina, umangofunika kulik- umba liwiro. Kulilowa banja: Kukwatira kapena kukwatiwa. Chitsanzo: Anzanutu analilowa banja. Kulima chidzulo: Kukalima madzulo dzuwa litapepa. Chitsanzo: Tiyeni tikalime chidzulo. Kulima pamsana: Kuchenjeretsana, kukhaulitsana. Chitsanzo: Mabwana anthu ndi amene akutilima pamsa- na. Kulimba m’maso: Kusagona msanga. Chitsanzo: Mwana ameneyu ndi wolimba m’maso. Kulimba mtima: Kupanda mantha, kusagonja. Chitsanzo: Ntchito ya ulonda imafuna kulimba mtima. Kulimba nazo: Kupirira, kuchita khama. Chitsanzo: Mwana ameneyu ndi wolimba nazo. 152