Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 145
Paphata pa Chichewa
phindu n’cholinga choti zinthu ziyambe kukuyendera
bwino.
Chitsanzo: (1) Ndipita kukagulitsa mandasiwa kuti
ndikokere. (2) Lero ndipitanso kukagulitsa kuti ndikokere.
Kukola chidwi: Kuchititsa chidwi kwambiri, kukopa.
Chitsanzo: Nsalu yachikasuyo ndi imene yakola chidwi
changa.
Kukolera:
(a) Kugwirira, kuyaka.
Chitsanzo: Sipanatenge nthawi yaitali kuti motowo
ukolere nkhalango yonse.
(b) Kukwanira, kufalikira.
Chitsanzo: (1) Tiyi wanuyu wakolera shuga. (2) Khalidwe
limeneli lakolera mudzi wonse.
Kukolezera moto (kusonkhezera): Kupangitsa kuti zi-
nazake zichitike kwambiri kapena zifale.
Chitsanzo: (1) Umphawi ndi umene ukukolezera moto kuti
ana ambiri ayambe uhule. (2) Akuluakulu a boma ndi
amene akusonkhezera anthu kuti azichita chiwawa.
Kukoma mtima: Kukhala ndi mtima wabwino, kuchitira
ena chifundo komanso kuwamvera chisoni.
Chitsanzo: Mayiwa ndi wokoma mtima.
Kukomedwa: Kusafuna kusiya chinthu, kutengeka ndi
zinthu.
Chitsanzo: Mayiwa ndi okomedwa.
Kukondera: Tsankho.
Chitsanzo: Mukugawa mokondera.
144