Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 144
Paphata pa Chichewa
Kukodza pamphasa: Kukodza ukamagona.
Chitsanzo: Anthu amene amakodzabe pamphasa atakula
amakhala kuti ali ndi matenda.
Kukoka chingwe: Kuimbira foni munthu wina.
Chitsanzo: Mukamva kuti mayeso atuluka, mukhoza
kungondikokera chingwe.
Kukoka ng’ona: Kuyenda ndi munthu wachimasomaso,
kutenga hule.
Chitsanzo: Bambo uja anakoka ng’ona dzulo, komatu ali
ndi mkazi kunyumba.
Kukoka nkhani: Kusafuna kusiya nkhani, kapena kuiko-
komeza.
Chitsanzo: (1) Kuti anthu amene akwatirana akhale ndi
banja losangalala amafunika kuyesetsa kuti asamakoke
nkhani. (2) Achimwene anu aja ndi amene akuikoka
nkhani.
Kukoka phazi: Kuyenda mofulumira.
Chitsanzo: Tiyeni tikoke phazi kuti tikafike kusanache.
Kukokanakokana: Kukanganakangana.
Chitsanzo: Anthu amenewa amakonda kukokanakokana.
Kukokera pambali: Kupita penapake kuti
mukakambirane.
Chitsanzo: Ndinawakokera pambali kuti ndiwatsine
khutu.
Kukokera:
(a) Kuchita zambiri.
Chitsanzo: Tiyeni tilimbikire ntchito kuti tikokere.
(b) Kupeza ndalama zambiri, kuchita zinthu kuti upeze
143