Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 118
Paphata pa Chichewa
n’kudzitosa nacho pathupi.
Chitsanzo: Kuphunzitsa ana a sukulu zinthu zomwe
sukuzidziwa kumakhala kudzibaya.
Kudzichekenira: Kudzitama, kunena zabwino zimene
umachita.
Chitsanzo: Atsikana safuna mnyamata wodzichekenira.
Kudzifufuza: Kuona bwinobwino zimene umalakwitsa,
kuganizira zimene umachita.
Chitsanzo: Udzifufuze bwinobwino kuti uone ngati uli ndi
khalidwe loipa.
Kudzigangira: Kusafuna kuuzidwa zochita, kudzitama.
Chitsanzo: Mfumu imeneyi ndi yodzigangira.
Kudzigobera manda: Kuchita zinthu zomwe zikhoza ku-
kubweretsera mavuto.
Chitsanzo: (1) Makutu a munthu akangotsekeka, ama-
khala kuti wayamba kale kudzigobera manda. (2)
Anayamba kale kufukula mwalawu ndipo lero wawaphin-
ja. Sankadziwa kuti akudzigobera manda.
Kudzigwira: Kudzilimbitsa mtima kapena kudziletsa kuti
usachita zinazake.
Chitsanzo: (1) Ndimafunika kudzigwira kuti ndisalire. (2)
Anandipsetsa mtima, kungoti ndinangodzigwira kuti ndi-
sawayankhe mwano.
Kudziipitsira: Kuchitira chimbudzi m’kabudula, kud-
zibibira, kudzinyerera.
Chitsanzo: (a) Atakumana ndi fisiyo anangotsala pang’ono
kudziipitsira. (b) Anamumenya kwambiri mpaka anad-
ziipitsira.
117