Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 117
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: (1) Mtsikana ameneyu wadyetsa amuna ambiri
uyu. (2) Amadyetsa kwa chikhwaya chapamtundapo.
Kudyetsedwa khuzumule: Kusiya kuyendayenda,
kufatsa.
Chitsanzo: (1) Masiku ano amangoti zungulizunguli pa-
nyumba yawo ngati anawadyetsa khuzumule. (2) Kufatsa
kumeneku sanawadyetse khuzumule awa!
Kudzadzada:
(a) Kukhapa chinthu.
Chitsanzo: (1) Zikungokhala ngati wina akundidzadzada
ndi musi. (2) Amudzadzada ndi chikwanje.
(b) Kumva kupweteka kwambiri.
Chitsanzo: Thupili likundidzadzada.
Kudzala:
(a) Kukwirira munthu kumanda kapena kuika maliro.
Chitsanzo: Bambo athu atamwalira tinabwera kuno ndipo
tinawadzala m’manda awo.
(b) Kudzadzitsa.
Chitsanzo: Madzi adzala mgolo.
(c) Kukwirira mbewu pansi kuti imere.
Chitsanzo: Tikupita kukadzala chimanga.
(c) Malo otayako zinyalala.
Chitsanzo: Mukataye kudzala.
Kudzandira: Kugwedezeka mofuna kugwa.
Chitsanzo: Amadzandira pobwera konseku, koma atafika
pamlathopa anadutsapo bwinobwino.
Kudzibaya: Kuchita zinthu zodzipweteka wekha. Tan-
thauzo lake lenileni ndi kutenga chinthu chakuthwa
116