Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 60
Ngale
Kino ndi mkazi wakeyu ankapita chakum’mwera n’kukasiya madindo a
mapazi, kenako n’kuloweranso chakumapiri kuja n’kumakayenda
pamiyala.
Anayenda mpaka miyendo kulowa m’mimba. Tsopano dzuwa linali
litayamba kulowa. Pofuna kupeza malo ogona, Kino anakwera mwala
wina ndipo chakuseri kwa mwalawo anawona malo ena obiriwira ndi
zomera. Pa nthawiyi madzi anali m’botolo aja anali atatha, choncho
ankafunikira madzi ena. Kino anaponya maso pamene panali zomerazo
ndipo anawona dziwe lamadzi. Posakhalitsa anakoka mkazi wakeyo
mpaka kufika pamwamba ndipo anayamba kuyenda motsata mwalawo
mpaka anakafika kumene kunali zomera zija. Pamene Kino ndi Juana
ankayenda motsatira mwalawo, ankatha kuwona dera lonse mpaka
kukafika kunyanja.
Kenako anatsika pamwalawo n’kufika padziwe lija. Zikuwoneka
kuti madzi a padziweli ankatuluka pakati pa mwala wina. Madziwa
ankayenda n’kumagwera kuchiphedi china. Akagwera kumeneko
ankangozimiririka osawonekanso. Chifukwa cha madziwa, pamalowa
pankabwera nyama zosiyanasiyana. Zina zinkayenda mtunda wawutali
zedi kuti zidzafike kumeneku. Nazonso nyama zolusa sizinkasowa pa-
malowa moti nyama zing’onozing’ono zikapusa, zinkajiwa
n’kunenepetsa zinzawozo.
Juana anali atatheratu ndi kutopa moti anangofikira kukhala pansi
n’kuyamba kusukusulitsa Coyotito yemwe anali thukuta lokhalokha.
Anatungiranso madzi m’botolo lija n’kumupatsa kuti amwe. Kino anali
ndi ludzu kwambiri moti anawerama padziwelo n’kuyamba kumwa
madzi ngati ngamila. Atamaliza anakhala pansi n’kumayang’ana Juana
akuyamwitsa Coyotito. Mphamvu zitabwerera, anadzuka n’kupita
kukasuzumira kumene ankachokera kuja. Koma ikakuwona litsiro si-
kata. Kino anawona anthu atatu aja akubwera chapatali.
Juana anatembenuka n’kuyang’ana mwamuna wake ndipo anawona
mantha amene analembeka pachipumi chake chosendeka chija.
“Bwanji bambo a Coyo?” anafunsa Juana.
“Anthu aja akubwera kuno! Ndikuganiza kuti posachedwapa afika
54