Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 59
Ngale
mwala chija ndipo Juana anawona mwamuna wakeyo akumuyangana
miyendo yake yomwe inali italembekalembeka ndi minga komanso
udzu. Nawonso mapazi ake anali atachekekachekeka ndi miyala yakuth-
wa. Powopa kumutayitsa mtima mwamuna wakeyo, Juana anaphimba
miyendoyo ndi siketi. Kenako anapereka botolo lamadzi lija kwa Kino
kuti aphe ludzu, koma Kino anakana. Chimenechi ndi chimene chinali
chochititsa chidwi ndi Juana. Ngakhale zinthu zithine bwanji, sankayi-
wala kuyika patsogolo zofuna za banja lake. Iye akanalolera kukhala ndi
ludzu, bola banja lake lonse limwe madzi. Komabe, kuthamanga ndi
mwana pansana kunja kukuwotcha kwambiri kunachititsa kuti thupi
lake lifowokeretu. Ngakhale ankafuna kubisa zimenezi, Kino
anazindikira.
“Juana,” anatero Kino, “Ineyo ndipitirizabe kuthawa, iweyo ubisale.
Anthuwa akufuna ineyo moti sindikukayikira kuti anditsatira m’mapiri-
wa. Chimene ndikufuna kuchita ndi choti, ndiwakope kuti anditsatire
kumapiri. Ukangozindikira kuti adutsa, iweyo ubwerere n’kuthawira ku
Loreto kapena ku Santa Rosalia. Ngati nditakwanitsa kuwazemba, ndi-
dzabwera kudzakufunafuna. Iweyo watopa kwambiri moti ndikuwona
kuti sikukhala kukuganizira ngati nditakuwuza kuti upitirizebe
kukwera chitundachi mwana ali kumbuyo. Imeneyi ndi njira yokhayo
imene ndingapulumutsireni.”
Juana anayang’ana mwamuna wakeyo momumvera chisoni.
“Ayi,” anatero. “Tiyeni tithawire limodzi.”
“Ineyo ndikhoza kupita patali kwambiri ngati nditakhala ndekha,”
anatero Kino. “Uyikatu moyo wa mwanayu pangozi ngati utapitiriza
kunditsatira.”
“Ayi,” anatero Juana.
Kino anayang’ana nkhope ya mkazi wakeyo kuti awone zizindikiro
za mantha, koma sanaziwone. Maso ake anali ngwe-e. Iye anali atalimba
mtima moti anapitirizabe kuyenda.
Posakhalitsa anayamba kuyenda pamiyala. Kino ankadziwa kuti
owasakasaka aja sangafike kumeneku. Zikanawatengera nthawi yayitali
kuti azindikire zoti kumeneko kwadutsa anthu. Pofuna kuwapusitsa,
53