Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 55
Ngale
ndi yamtengo wapatali. Ikanakhala kuti si yamtengo wapatali si bwenzi
akulimbana nafe.”
“Kodi amene anakuwukirani usiku uja mukumudziwa? Kapenatu
nayenso anali wogula ngale?”
“Mwina,” anatero Kino. “Kungoti sindinamuwone nkhope.”
Kino ankati akayang’ana ngaleyo ankawona tsogolo lake lonse.
“Tikagulitsa ngaleyi, tigula mfuti,” anatero Kino, ndipo ankayan-
g’ana ngaleyo kuti awone mfutiyo, koma m’malo mwake ankangowona
dothi la pamene anakhalapo likuwonekera pangaleyo. Dothi lake linali
lofiyira psu-u. Kenako anati, “Tikagulitsa ngaleyi tipeza ndalama zoti
tikamangitsire ukwati wathu kutchalitchi. Tipezanso ndalama zoti tilipi-
rire mwana wathuyu sukulu. Ndikufuna kuti Coyotito aphunzire
kuwerenga,” anapitiriza motero mawu ake akumveka mwankhawa. Iye
anali atakumbukira kuti dokotala uja anamupatsa Coyotito mankhwala
oyipa n’cholinga choti atenge ngaleyo. Ngakhale dokotalayo ankafuna
kuwaphimba m’maso, Kino anam’tulukira.
Kenako anayikanso ngaleyo m’thumba. Nyimbo ya ngale ija ina-
yamba kumveka modabwitsa m’mutu mwake ndipo inkangokhala ngati
nyimbo yoyipa.
Tsopano kunja kunangoti ju-u. Chifukwa cha kuwotcha kwa dzuwa,
Kino ndi Juana anathawira pakanthunzi kena. Pamenepo Kino anagona
pansi n’kuphimba nkhope yake ndi chisoti.
Koma Juana sanagone. Anangokhala du-u ngati chulu. Tsaya lake
linali likumuwawabe pamene anawombedwa mbama paja. Koma Juana
anali mkazi wopirira. Anali atatsimikiza mtima kukhalabe ndi mwamu-
na wake zivute zitani. Coyotito atadzuka, anamuyika pansi patsogolo
pake ndipo anayamba kusewera. Chifukwa cha kutentha, Juana
anatenga botolo la madzi n’kumupatsa kuti aphe chipemba.
Koma mwadzidzidzi, Kino anayamba kubwebweta moti anadzi-
muka akulira mokweza. Zinkangokhala ngati winawake amafuna ku-
mupha kutuloko. Mkazi wake anachita mantha kwambiri. Mtima wake
utakhala pansi, Kino anayamba kumvetsera zochitika mozungulira pa-
malopo. Chomwe anamva m’mutu mwake kunali kutentha kong’amba
49