Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 54

Ngale atamva kuthamanga kwa nyamazo anagwira mwamphamvu mpeni wake. Mpeni umenewu unkachititsa kuti azidzimva wotetezeka. Nyimbo ya ngale ija inayambanso kulira m’mutu mwake ndipo cha- pansipansi ankamvanso kulira kwa Nyimbo ya Banja Lake. Kunja kusa- nache, Kino anasakasaka malo pafupi ndi nsewuwo kuti aphe tulo. Ana- peza malo ena pafupi ndi nsewuwo pomwe panali ziyangoyango. Miten- go ina ikuluyikulu inkabisa malowa. Kenako Juana anakhala pansi n’kuyamba kuyamwitsa mwana wake ndipo Kino anabwereranso ku- nsewu kuja. Iye anathyola nthambi ya mtengo n’kuchotsa zizindikiro zonse zomwe zikanachititsa anthu kuganiza kuti pamalopo pabisala an- thu. Kunja kutangoyamba kuwala, Kino anamva kulira kwa galimoto ikudutsa munsewu uja ndipo anakhala pansi n’kumayiyang’ana ikudu- tsa. Kenako anabwereranso kunsewuko ndipo anapeza kuti madindo a mapazi awo aja afufutika ndi mateyala a galimotoyo. Zimenezi zinamu- khazika mtima pansi moti anathyolanso nthambi ina n’kuyamba kufufu- ta zizindikiro za mapazi ake kwinaku akubwerera kumene kunali Juana. Juana anatenga mikate ingapo yomwe Apolonia anawapangira n’ku- mupatsa mwamuna wake. Chifukwa chotopa ndi ulendowo, Juana ana- gona pang’ono. Koma Kino sanagone. Atamaliza kudya anangozyolikira pansi n’kumaganiza. Posakhalitsa dzuwa linayamba kukwera. Tsopano anali kutali ndi nyanja ndipo kunja kunayamba kutentha ngati ng’anjo. Pamene Juana ankadzuka, dzuwa linali lili paliwombo. “Mukuganiza kuti angatitsatire mpaka kuno?” anafunsa Juana. “Anthu aketu ndi zilombo. Akhoza kutilondola kulikonse,” anatero Kino. “Sangalephere kutitsatira akudziwa kuti tili ndi ngale.” Atanena zimenezi, Juana anati, “Mwinatu ogula ngale aja amanena zowona. Bwanji ngati ngaleyi ilidi yachabechabe?” Kino anapisa m’malaya ake n’kutulutsa ngale ija. Dzuwa linkachititsa kuti ngaleyo iziwala kwambiri moti inkamuthobwa m’maso. “Ayi,” anatero Kino, “anthu aja ndi akuba. Akudziwa kuti ngaleyi 48