Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Seite 38

Ngale “Imeneyi ndi ngale yamtengo wapatali kwambiri. Palibe ana- wonaponso ngale yangati imeneyi,” anatero Kino. “Ngale imeneyi yakulitsa,” anatero wogulayo. “Ndi ndani angagule ngale yayikulu chonchi? Kunja kunotu kulibe makasitomala omwe ama- gula ngale zazikulu ngati zimenezi, moti ndikutsine khutu mnzanga: ngaleyi ndi yopanda ntchito mpang’ono pomwe. Apa ndiye zakuvuta kwabasi.” Nkhope ya Kino inasinthiratu ndi mkwiyo. “Ngaleyitu ndi yamtengo wapatali,” anatero Kino. “Palibe anayamba wapezapo ngale ngati imeneyi.” “Koma vuto lake ndi loti yakulitsa,” anatero wogula uja. “Ndi ngale yabwinodi ndithu, vuto ndi kukulako basi. Mokuganizira ndikhoza ku- kupatsa 1,000 pesos kuti ndiluze ndi ineyo.” Nkhope ya Kino inayamba kuwoneka mowopsa. “Mtengo wa ngale imeneyi ndi 50,000, inuyonso mukudziwa zimenezo. Mukufuna mun- gondibera basi!” Wogula uja anamva phokoso losasangalatsa kuchokera m’khamu lija ndipo nayenso anayamba timantha. “Ngati sukugwirizana ndi zimene ndikukuwuzazi,” anatero mofu- lumira, “pita ukafunse ogula akumtundako. Alvaro!” anayitana wogula ngale uja, ndipo wantchito wake anasuzumira pakhomo, “Tapita ukayitane ogula ngale atatu a pamtundapo. Koma usakawawuze chimene ndikuwafunira. Ukangowawuza kuti abwere mwansanga.” Gulu la anthu linamuperekeza Kino lija linayamba kukambirana chapansipansi. Kunena zowona ngale ya Kino inalidi yayikulu kwambiri mosiyana ndi ngale zina komanso inali ndi mtundu wachilendo. Iwo ankawona kuti 1,000 pesos ndi ndalama yambiri kwa munthu wosawu- ka ndi mano omwe ngati Kino. Iwo ankakumbukira kuti dzulodzuloli Kino analibiretu olo 1 tambala ndipo ankawona kuti n’kupusa kutaya mwayi wanzama ngati umenewo. Koma Kino anamenyetsa nkhwangwa pamwala. Pa nthawiyi ankan- gomva ngati mizimu yoyipa yamuzungulira ndipo nyimbo yoyipa inka- mveka m’makutu mwake. Ngaleyo inali idakali patebulo paja ndipo diso 32