Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 37
Ngale
muzilowa kamphepo komanso kuwala. Pa nthawiyi ankayimba mulizi
kwinaku akuyang’ana kukhomo. Kenako anangozindikira Kino watulu-
kira, chigulu chija chikumutsatira pambuyo.
“Ndakulandira m’bale wanga,” anatero munthu wonenepayo maso
ake akuwoneka ngati a Yudasi. “Khala omasuka ndithu, ine ndili pano
kuti ndikuthandize.”
Koma kenako nkhope ya wogulayo inasintha. Iye ankasekerera ndi
mbali imodzi ya kamwa lake ndipo maso ake olowa mkati, omwe
ankawoneka ngati akusuzumira m’chigompholera, anayamba
kuyang’ana mocheka ndi mwano.
“Ndabwera kudzagulitsa ngale yanga,” anatero Kino. Juan Tomas
anali pambali pake ndipo anthu ankamutsatira aja ankasuzumira pakho-
mo. Ana ena ankakwera pazenera n’kumasuzumira.
“Uli ndi ngale imodzi basi?” anatero munthu wonenepa uja.
“Anzakotu amabweretsa mulu wa ngale, mwina 12 pakamodzi. Tulutsa
ngale yakoyo tiyiwone. Ndikugula pamtengo wabwino kwambiri.”
Mwapang’onopang’ono Kino anatulutsa kachikwama anayika ngale
kaja. Mkati mwa kachikwamako anatulutsamo kansanza kofewa. Ndipo
mkati mwa kansanzako munatuluka ngale yamtengo wapatali ija.
Atangoyiyika patebulo, wogulayo anadula mpumo wake ndipo pa-
kamwa pake panayasama ngati ng’ona. Ndalama ankaseweretsa ija in-
amupulumuka n’kugwera pansi. Maganizo ake atabwereramo, wo-
gulayo anatola ngale yamtengo wapataliyo n’kuyamba kuyiyang’ana
ngati akufuna kuyilowetsa m’maso.
Kino anadikirira ndipo gulu la anthu anabwera nalo lija nalonso
linadikira. Ena ankanong’onezana kuti:
“Akadayiyang’ana. Zikuwoneka kuti sanayambe kukambirana
mtengo.”
Wogulayo anaponya ngale ija patebulo mokhala ngati ikumunyansa.
Nkhope yake inasinthiratu n’kukhala pakatikati pa kukhumudwa ndi
kumwetulira kwawutambwali.
“Pepa m’bale wanga,” anatero wogulayo.
31