Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Página 22
Ngale
Gawo 3
Tawuni imakhala ngati chinthu chamoyo. Imakhala ndi mutu, mapewa
komanso mapazi ndipo matawuni awiri samakhala ofanana. N’zoda-
bwitsa kwambiri mmene nkhani imafalira m’tawuni. Nkhani yatsopano
imathamanga kwambiri kuposa mphenzi ndipo imakolera paliponse
m’kanthawi kochepa, makamakanso nkhaniyo ikakhala yokhudza mun-
thu amene anthu samamuganizira. Ndi mmenenso zinalili ndi nkhani ya
Kino. Inayenda mofulumira n’kufika paliponse ngati mpweya.
Kino ndi Juana asanafike ndi kunyumba kwawo komwe, anthu anali
atayigula kale nkhaniyi. Paliponse anthu ankakambirana za ngale yo-
mwe Kino anapeza ndipo nkhaniyi inayenda mpaka m’tawuni, kunyum-
ba zamabwana kuja. Inafikanso kwa wansembe yemwe ankawongola
miyendo pafupi ndi tchalitchi chake. Wansembeyo atangomva nkhaniyi,
nthawi yomweyo anakumbukira ming’alu yomwe inali patchalitchi
chake komanso zinthu zambirimbiri zomwe zinkafunika kukonzedwa.
Iye ankawona kuti ngati nkhosa yake yapeza ngale yamtengo wapatali,
ndiye kuti ikufunika kupereka kenakake kutchalitchi. Anakumbukiranso
kuti Kino ndi mkazi wake sanamangitse ukwati wovomerezeka wa
kutchalitchi komanso kuti mwana wawo Coyotito anali asanabatizidwe.
Izi zinachitika chifukwa analibe ndalama zolipirira wansembeyo kuti
awayendetsere dongosolo la zochitikazi.
Nkhaniyi inayenda ndi mapazi n’kukafikanso kwa ogulitsa
m’mashopu. Iwo anayamba kuyang’ana zovala zawo zomwe zinkathera
mualumali chifukwa chosowa wogula. Inafikanso kwa dokotala uja
yemwe ankathandiza mayi wina wachikulire. Vuto la mayiyu linali uka-
lamba basi. Koma dokotalayo sanamuwululire zimenezi. Ankangomu-
kulitsira mavuto ake n’cholinga choti alipire zambiri. Dokotalayu ata-
ngozindikira kuti Kino ndi amene anabwera ndi mwana m’mawa uja,
nkhope yake inasintha ndipo ananena kuti, ”Dokotala wa mwana ame-
neyo ndine! Kuteroko anabwera kuno kuti ndidzamupatse mankhwala a
poyizoni wapheterere m’mawawu.”
Nkhaniyi inafikanso kwa opemphapempha aja ndipo nawonso
anayamba kufuwula mwachimwemwe. Ankati munthu wosawuka
akatola chikwama sawumira pothandiza ovutika.
16