Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 52

Ngale ndi mchimwene wakeyo. “Ndiye mulowera kuti?” “Tilowera kumpoto,” anatero Kino. “Ndinamva zoti kumpoto kuli matawuni ena.” “Koma usadutse m’mbali mwa nyanja,” anatero Juan Tomas po- muchenjeza m’bale wakeyo. “Anthu akukonza zoti akakusakesakeni ku- meneko. Kodi ngale ija ukadali nayo?” “Inde, ndili nayo,” anatero Kino. “Ndayisunga mosamala. Ndikud- ziwa kuti ndi imene yandiputira mavuto onsewa. Koma sindiyitaya ayi,” anatero Kino diso lili pamtunda. “Panyanja pali chimphepo chowopsa,” anatero Juan Tomas. “Umenewu ndi mwayi wako chifukwa anthu amene angayambe kuku- londolaniwo azingopupulika. Sakwanitsa kuwona mafulufutu a mapazi anu chifukwa azingofufutika ndi mchenga.” Kino ndi mkazi wake ananyamuka mwezi usanatuluke, chimdima chili bo-o. Juana anabereka Coyotito kumbuyo ndipo mwanayo anali m’tulo tofa nato. Juan Tomas anakumbatira komanso kupsopsona Kino. Kunena zowona, zinkangokhala ngati pachitika maliro. Kenako ana- muwuza kuti, “Mulungu akhale nawe m’bale wanga. Koma ukunenetsa- di kuti suyitaya ngaleyo?” “Ukuganiza kuti ndikayitaya nditsala ndi chiyani?” anafunsa Kino. “Kutaya ngaleyitu n’chimodzimodzi kutaya moyo wanga. Basi tapita, nawenso Mulungu akhale nawe.” 46