Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 51

Ngale tibiseko m’bale wanga.” Pamene Kino ankayang’ana mchimwene wakeyo anawona kuti anali ndi nkhawa yayikulu. “Sikuti mutibisa kwa nthawi yayitali,” anapitiriza motero Kino. “Popeza kunjaku kwacha kale, mungotibisako masanawa, kukangoda ti- nyamuka tidzipita.” “Chabwino, tikubisani,” anatero Juan Tomas. “Sitikufuna kuti tikuyikeni m’mavuto,” anatero Kino. “Tikamachoka kuno tinyamuka ndi usiku kuti anthu asatiwone.” “Usadandawule m’bale wanga, tili pano kuti tikutetezeni,” anatero Juan Tomas. Kenako anatembenukira kwa mkazi wake, “Apolonia, tseka chitseko. Usawuze aliyense kuti Kino ndi banja lake ali kuno.” Anabisala tsiku lonse m’nyumbamo. Kino ndi mkazi wake ankatha kumva anthu a nyumba zapafupi akukambirana za iwo. Moto uja utazi- lala, anthu anayamba kufufuza m’phulusa matupi awo koma sanapeze kanthu. Ena anathamangira kudoko kukayang’ana bwato la Kino koma analipeza litadzadza madzi, pansi pake pali chim’bowo chachikulu. Juan Tomas anapita kukakambirana nawo. Iye anawuza m’modzi wa iwo kuti, “Ndikuganiza kuti Kino ndi Juana athawira kum’mwera podutsa m’mbali mwa nyanja. Akuyesa kuthawa masoka amene akutsata banja lawo.” Anawuzanso wina kuti, “Kino sangasiye nyanjayi n’kupita kwina. N’kutheka kuti wapeza bwato lina.” Kenako ananena kuti: “Ndikudera nkhawa mkazi wanga Apolonia, ali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha zimene zachitikazi.” Tsiku limenelo, panyanja panachita chimphepo chowopsa moti palibe anapita kosaka ngale. Kenako Juan Tomas anayamba kuwuza an- thu kuti, “Ndikuda nkhawa kuti mmene nyanja yakwiyiramu ikhoza ku- wameza.” Juan Tomas ankati akamapitanso kunyumba kwake kuja an- kapita atanyamula zinthu zomwe wabwereka mwa anzake. Ulendo wina anapita ndi thumba la chakudya komanso mpeni wawutali. Mafunde owopsa anali akuwumbudza mchenga wapagombelo. Mphepoyi inathamangitsa mitambo yonse n’kuchititsa kuti kumwamba kuyere mbee. Chakumadzulo, Juan Tomas anagwetserana mumchenga 45