Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 20
Ngale
kamba ankatolerazo munalidi ngale? Kino ankadziwa kuti m’bwato lom-
we linkayandama pamwamba pake, Juana ankapempherera mwayi. Iye
ankafuna ngale yoti akayigulitsa apeze ndalama zokalipira dokotala uja.
Zimenezi zinkafunikadi mwayi chifukwa nthawi zina ankatha kuswera
tsiku lonse, koma osapeza ngale ngakhale imodzi. Ndiye popeza pa
nthawiyi anali akusowa mtengo wogwira, Nyimbo ya Chiyembekezo
inayamba kumveka kwambiri m’mutu mwa Kino.
Kino anali adakali wachinyamata komanso wamphamvu, moti anka-
tha kukhala pansi pa nyanja kwa mphindi zambiri. Iye ankagwira ntchi-
to yakeyi mofatsirira ndipo ankasankha zikamba zikuluzikulu zokhazo-
kha. Pafupi ndi dzanja lake lamanja, anawona chikamba chachikulu
modabwitsa chili pachokha. Chikambachi chinali chotseguka pang’ono
ndipo mkati mwake munali kenakake kowala. Koma pamene ankati azi-
chitola, chikambacho chinatsekeka. Kino anachitola mwansanga n’ku-
chiyika m’thumba muja. Kenako anasiya mwala unkamuthandiza kuti
akhale pansi pamadzipo n’kusambira kupita pamwamba. Posakhalitsa
anatulutsa mutu wake ndipo tsitsi kale lakuda linanyezimira ndi dzuwa
lomwe linkawomba m’mawawo.
Kino anaponyera thumba lija m’bwato ndipo nayenso anakwera.
Nkhope yake inali ikuwala ndi chisangalalo. Juana anazindikira chimene
chinkachititsa kuti Kino aziwoneka wosangalala, moti anayang’ana kum-
bali. Juana anali wodabwitsa kwambiri. Tikutero chifukwa ankakhulu-
pirira kuti si bwino kumafunitsitsa chinthu chinachake. Ankawona kuti
ukamachifunitsitsa mpamene chimamera mapiko n’kuwuluka. Ankadzi-
wanso bwino kuti mtima wadyera umasonyeza mwano kwa milungu
ndipo ikakwiya imangokuchotsera mwayiwo kuti ukhawule.
Mosamala kwambiri, Kino anatulutsa mpeni wake wawufupi
n’kuyamba kukanula zikamba zazing’onoko zija. Ankafuna kuti chikam-
ba chachikulucho achikanule pamapeto. Choncho anayamba kutulutsa
zikamba zing’onozing’ino zija n’kumazikanula ndipo akapeza kuti
mulibemo kanthu, ankaziponyeranso m’nyanja. M’zikamba zimenezi
sanapezemo kanthu. Kenako anatenga chikamba chachikulu chija n’ku-
machiyang’ana ngati wangochiwona kumene. Kunena zowona, Kino
ankadziwa kuti mkati mwa chimambacho muli kanthu kapadera ndipo
14