Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | 页面 9

Ngale kuwalako kusamuthobwe m’maso. Tsopano ankatha kumva mkazi wake akuwumba mikate ndipo posakhalitsa kafungo kokodola njala kanafika pamphuno zake. Pa nthawiyi kunatulukira galu wina wowonda mo- chititsa mantha. Galuyo anapita kukagona pafupi ndi Kino. Kunena zowona kunja kunacha bwino kwambiri ngati mmene zinkakhalira masiku onse. Atamaliza kupanga mikate, Juana anachotsa Coyotito m’bokosi ankamugoneka muja ndipo anayamba kumusambitsa. Atamaliza ana- mukutira ndi shawelo n’kuyamba kumuyamwitsa. Kino anali atazolow- era kuwona mkazi wakeyu akuchita zimenezi moti ngakhale anali panja, ankatha kuwona zonsezi m’maganizo mwake. Posakhalitsa Juana anayamba kuyimbira mwana wakeyo kanyimbo komugonekera. Nyim- boyi inali yakale kwambiri ndipo inkamutonthoza akamalira. Nyumba yawoyi inali kumpanda wawudzu. Mpandawu unagundi- zana ndi mipanda inanso yomwe mkati mwake munali nyumba zawudzu. M’mawawu, m’nyumba zimenezinso munangoti utsi tolo-o. Chimenechi chinali chizindikiro choti anthu akukonza kadzutsa. Koma zochitika m’nyumba zimenezi sizinali nyimbo ya Kino. Tikutero chifu- kwa amuna a makomo amenewo anali ndi mavuto awo, komanso nkhumba zawo. Ngati anali ndi mkazi, mkazi wawo anali wina, osati Juana. Kino anali mwamuna wadzitho ndipo m’mutu mwake munali tsitsi lakuda lomwe linkagwera pachipumi chake choyera mwachimwenye. Nthawi zina maso ake ankawoneka awubwenzi, koma nthawi zina ankawoneka owopsa ngati a chimbalangondo. Analinso ndi ndevu za- pamlomo zowoneka ngati chotsukira mbale. Popeza tsopano dzuwa linali litakwera, Kino anachotsa bulangete linali kumutu lija ndipo ana- yamba kuyang’ana atambala awiri omwe ankafuna kusosolana, mitu yawo atayilozetsa pansi, nthenga zam’khosi zitafufuma ndi ukali. Kino anayang’ana nkhukuzo kwa kanthawi chidwi chake chisanachoke n’ku- tembenukira kwa nkhunda zomwe zinkawuluka chapatali. Chilengedwe chonse chinali chitadzuka tsopano, ndipo Kino anayimirira n’kukalowa m’nyumba. Pamene ankalowa, Juana anadzuka n’kukagoneka Coyotito m’bokosi 3