Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 10
Ngale
lake lija. Kenako anayamba kupesa tsitsi lake n’kulimanga kumbuyo ndi
maliboni obiriwira. Kino ananjuta pafupi ndi moto n’kumadya mikate
yake. Atamaliza kudya, anatenga kapu ya madzi n’kumwera. Juana
nayenso anabwera n’kudya mikate yake. Chichereni, anthuwa anali
atangoyankhulana kamodzi kokha basi. Iwo sankawona chifukwa cho-
mangokhalira kukamwa mbe-e ndi nkhani zosafunika kwenikweni.
Nthawi zambiri ankangoyankhulana ndi maso. Kino anapuma mwam-
phamvu ndipo ichi chinali chizindikiro choti wakhutira ndi zimene mka-
zi wakeyo wachita. Onse ankawoneka osangalala.
Tsopano dzuwa linayamba kukwera moti kuwala kwake kunadutsa
m’ming’alu komanso mipata ing’onoying’ono ya nyumba ya Kino. Ku-
walako kunkangokhala ngati mapayipi ataliatali m’nyumbamo ndipo
kwina kunalunjikanso pabokosi la Coyotito komanso pazingwe zomwe
zinamangiriridwa kudenga zija. Kuwala kumeneku n’kumene kunathan-
diza Kino ndi Juana kuwona chinthu china chomwe chinkayenda
pachingwe chimodzi cha bokosilo. Thupi la Kino ndi Juana
linangowumiratu atawona chinthucho. Mmene chinkayendera, zinali
zowonekeratu kuti ndi pheterere.
Kino anapuma mwaphokoso zedi chifukwa chankhawa ndipo po-
funa kuti phokoso la mpumowo lisadzidzimutse pheterereyo, anayamba
kupumira mkamwa. Kenako anapitirizabe kuyang’ana pheterereyo thupi
lake litawuma ngati mtembo. M’maganizo mwake munali mutayamba
kumveka nyimbo yachilendo. Imeneyi inali nyimbo yoyipa, nyimbo ya
mdani, nyimbo yowopsa. Nyimbo ya Banja Lake ija inali itasiya kulira.
Pheterereyo anatsetserekabe ndi chingwecho mchira wake uli m’mwam-
ba. Juana anayamba kupemphera chapansipansi. Iye ankapempha mi-
lungu yamakolo ake kuti ithamangitse tsokalo. Kuwonjezera pamenepa,
ankayitananso Mariya Woyera kuti ateteze mwana wakeyo. Ankachita
izi posadziwa kuti chipulumutso chichokera kuti. Pa nthawi imeneyi Ki-
no anayamba kuyenda ngati akuponda pamoto n’kumalowera kunali bo-
kosi kuja. Maso ake anangoti ga pa pheterereyo. Koma zimene zimachi-
tika nthawi zina zimakhala kamba anga mwala. Zimene Coyotito anachi-
ta pamenepa zinali zoti sungaziyembekezere. Zoti makolo ake anali
akugwa ndi mapemphero powopa pheterereyo analibe nazo ntchito.
4