Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 247
Miyambi ya Patsokwe
Waba nkhukhu ndamuona, sindimutchula chifukwa choti
ndili ndekha.
-Mawuwa amatanthauza kuti amene walakwa ndikumudziwa,
koma poti palibe amene amagwirizana nane pamudzi pano, sin-
ditchula.
Wabisa mbuzi m’munda.
-Kumeneku ndi kusunga mavuto, mwachitsanzo kusunga waku-
ba m’nyumba.
Wachaje ndi gaga wowawa, sasipika.
-Mawuwa amatanthauza kuti anthu adera amakhala ngati gaga
wowawa, yemwe nsima yake sungadye yosipa. Anthu ena
amangofuna kuwathandiza basi koma sangakuthandize
zitakuvuta.
Wachake ndi wachake.
-Munthu amene ali ndi khalidwe loipa saleka.
Wachake sachileka.
-Munthu amene ali ndi khalidwe loipa saleka.
Wachedwa ndi makonkhwa.
-Makonkhwa ndi zinthu zopanda pake. Mawuwa amanenedwa
ngati munthu wina wachedwa chifukwa cha zinthu zopanda
pake.
Wachenjera atalumwa.
-Munthu amachenjera atalumwa kapena kuti atalumidwa ngati
anthu ena, kaya alendo, amuchitira chipongwe. Akazindikira
chipongwecho amati, “ndachenjera nditalumwa,” zomwe ziku-
tanthauza kuti wachenjera zitaipa kale.
Wachenjeza ng’anga, chilonda chisanapole.
-Mawuwa amanena za sing’anga, kapena kuti dokotala amene
akukupatsa mankhwala oti uchire bala lako, koma iweyo
246