Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 246
Miyambi ya Patsokwe
Uyenda liti mwana wosayenda nsangawe, utimalizira zam’nk-
hokwe.
-Kuchita zinthu mwachangu n’kofunika kuopa kuti ntchito
idzakupanikize nthawi imodzi.
Uyo waona matumbuzi, nyama ndi yake.
-Chimene wapeza pogwira ntchito ndiye chako. Si bwino ku-
machenjeretsa anthu ena. Matumbuzi ndi mbalame zomwe zim-
akonda kudya nyama zakufa, ndiye ngati waona matumbuziwo,
nyama imene akufuna kudyayo ndi yako.
Uzikhoma chitseko chako kuti anthu apafupi asakhale akuba.
-Zimene timachita zingachititse kuti anthu ena akhale okhulupi-
rika kapena ayi. Mwachitsanzo, kumangosiya katundu wathu
paliponse kungachititse kuti anthu akopeke n’kusanduka akuba.
Vuto la Phwiti, akakhuta salawira mtondo.
-Pali anthu ena ukawachitira zabwino amangoti zii, osayamikira
zimene wawachitira. Amaoneka akakhala kuti akufuna
chinachake basi.
245