Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 229
Miyambi ya Patsokwe
pamakhala ziyeso zambiri zingakukope kuti uchokepo pabwino-
po.
Ukakhala wopanda chala usamadane n’kuloza.
-Ngati sungathe kugwiritsa ntchito chinthu usamadane ndi ame-
ne angathe.
Ukakhala wopanda chala, usamadane n’kuloza.
-Tisamapondereze mwayi wa anzathu chifukwa choti tilibe.
Ukakhala wopanda galu, umalimba ndi mpiringidzo.
-Munthu amene alibe galu pakhomo amafunika kukhoma
chitseko chake. Kale ankagwiritsa ntchito mtengo kapena kuti
mpiringidzo poteteza kuti chitseko chawo chisatseguke chisawa-
wa. Tizidalira zimene tili nazo. Ngati tilibe galu, mtengo kapena
mwala zingathandize kupirikitsa akuba.
Ukakhala wopanda kanthu, dziko umalidyera ku uchi.
-Ngakhale munthu wosowa, pa masiku a phwando nayenso
amadyako zabwino.
Ukakhala wopanda mano usamaswe phale.
-Ngati sungathe kugwiritsa ntchito chinthu usamadane ndi ame-
ne angathe.
Ukakhala wopanda mano, usamaswe phale.
-Ifeyo zikatikanika, tisamatsekereze mwayi wa anzathu.
Ukakhala wopanda mng’oma umadya mavu.
-Munthu amapeza zinthu zogwirizana ndi zomwe ali nazo.
Munthu wopanda mng’oma sangadye uchi.
Ukakhala wopanda tsitsi, usamabise lumo.
-Tisamapondereze anzathu koma tiwapatse mwayi wokhala ndi
zomwe akufuna.
Ukakhuta pachika, ana apano sakhuta.
-Ukakhala ndi zinthu kumasunga chifukwa mawa
228