Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 228
Miyambi ya Patsokwe
Ukafuna kupha galu umapezeratu mtengo.
-Ndi bwino kupezeratu zinthu zonse zofunika usanayambe
kugwira ntchito.
Ukaipa dziwa nyimbo.
-Palibe munthu amene amadziwa zonse kapena amene ali ndi
zonse zofunikira. Zikakuvuta zina umafunika kusakasaka
zimene umachita bwino n’kumachita zimenezo.
Ukaipa nkhope, dziwa kuvina.
-Palibe munthu amene amadziwa zonse kapena amene ali ndi
zonse zofunikira. Zikakuvuta zina umafunika kusakasaka
zimene umachita bwino n’kumachita zimenezo.
Ukaipa nkhope, dziwa nyimbo.
-Palibe munthu amene amadziwa zonse kapena amene ali ndi
zonse zofunikira. Zikakuvuta zina umafunika kusakasaka
zimene umachita bwino n’kumachita zimenezo.
Ukakalamba usamabise lumo kuti ena asametere.
-Tisamapondereze anzathu koma tiwapatse mwayi wokhala ndi
zomwe akufuna.
Ukakhala kwa eni umafunika kukhala nkhosa.
-Munthu ukakhala kwa eni umayenera kufatsa. Ukamachita
matukutuku amakuthamangitsa.
Ukakhala m’mwamba usamatukwane pansi, ungadzasowe
wokutola ukagwa.
-Osamanyoza anzathu tikakhala pabwino.
Ukakhala mwana, mphanje umayambira pamchenga.
-Ukafuna kuphunzira kuchita zinazake, umafunika kuyamba
ndi chophweka.
Ukakhala pabwino, poipa pamakuitana.
-Mwayi suchedwa kutha. Nthawi zina ukakhala pabwino
227