Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 212
Miyambi ya Patsokwe
Sadya galu adam’dula mlomo.
-Munthu wina ankanena kuti sadya galu. Koma tsiku lina anthu
anamupeza akutsuka m’kamwa ndi galu yemweyo ndipo
anamudula mlomo. Tisamaneneretu kuti chakuti sindingachite
chifukwa tsiku lina tingadzachite manyazi anthu atatipeza tiku-
chita zomwezo.
Sadyeka adadyeka ndi ndi mafupa omwe.
-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo chifukwa tingachite
manyazi ena atatiposa. Mwachitsanzo, munthu amene
amadzitama kuti amadziwa ndewu, anzake ena akhoza ku-
muphwasamula.
Sadyeka adamudya ndi nyanga zomwe.
-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo chifukwa tingachite
manyazi ena atatiposa. Mwachitsanzo, munthu amene
amadzitama kuti amadziwa ndewu, anzake ena akhoza ku-
muphovomora.
Sadyeka anadyeka ndi mafupa omwe.
-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo chifukwa tingachite
manyazi ena atatiposa. Mwachitsanzo, munthu amene
amadzitama kuti amadziwa ndewu, anzake ena akhoza ku-
muphovomora.
Safunsa adadya phula.
-Munthu wina adadya phula m’malo mwa uchi chifukwa cho-
safunsa. Kufunsira nzeru kwa ena si kupusa, kumathandiza kuti
uchita zinthu moyenera.
Safunsa adafera m’chipululu.
-Ngati munthu sungafunse njira m’chipululu, ukhoza kufera
momwemo. Ndi bwino kumafunsa ngati sitikudziwa chochita,
kusiyana n’kungochitabe, kenako n’kukumana ndi mavuto.
211