Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 211

Miyambi ya Patsokwe kumupatsa zabwino. Ukamupatsa nthuli yabwino amatayira agalu. Pondupondu, njira idzera momwemo. -Zomwe munthu umachitachita zimasanduka chizolowezi. Nga- ti umachita zoipa zimakulowerera, chimodzimodzi ukamachita zabwino. Popanda nkhuni moto sumayaka. -Nkwiyo uli ngati moto, ukakhazikika pamikangano komanso kumaputa anzako moto umayaka. Anthu amatha kumenyana chifukwa chosaugwira mtima. Potepote mpoyamba, potsiriza ndi chingwe. -Zinthu zina zimayamba pang’onopang’ono pomaliza n’kukhala zazikulu. Mwachitsanzo, kuti vuto lichitika, pamakhala kuti pa- khala pakuchitika zambiri zomwe anthu ankazinyalanyaza. Psi! luma! n’kukhala ndi mbuyake. -Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina amakonda kudalira mphamvu za ena. Pusepuse ulandira mpeni. -Munthu sukhala wochenjera pa chilichonse, tsiku lina anthu amakugwira n’kukukhaulitsa. Pusi adafa m’njakata. -Tsiku lina pusi ankafuna kugwira zingwe ziwiri nthawi imodzi moti anasokonezeka n’kugwera pansi moti anathudzuka. Siz- imatheka kuchita zinthu ziwiri nthawi imodzi. Nthawi zina umafunika kusankha chimodzi. 210