Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 197
Miyambi ya Patsokwe
Odwala agawa mphika.
-Mawuwa amanena za munthu amene amakonda kupezeka
pamene pali zabwino, osati pamene pali mavuto.
Okazinga nthanga akazingira a mano kuti akukute.
-Si bwino kuchitira nsanje ena akamathandiza anzawo kuti
atukuke. Anthu amachitira zabwino anthu omwe akuoneka kuti
ali ndi tsogolo, m’mawu ena ali ndi mano oti akhoza kukukuta.
Okoma apitana.
-Zabwino zimene timachitira ena zimachititsa kuti ena azitichit-
ira zabwino.
Okoma atani onga Fungwe.
-Anthu ena umatha kuwachitira zabwino koma sayamika. Nya-
ma ya Fungwe inali yosowa kwambiri moti ena amati akapatsid-
wa nyamayi amathokoza. Tiyenera kumathokoza wina
akatikankhira patsogolo.
Osachulutsa gaga m’diwa.
-Osachulutsa zonena zingasokoneze zinthu. Munthu akaika ga-
ga wambiri m’diwa, mbewa imakhutsa isanafike padiwalo.
Osagula phazi la Njovu.
-Kungoona phazi la njovu sindiye kuti taona njovu. Si bwino
kumagula malonda omwe sunawaone. Si bwino kumachita zin-
thu mwaphuma komanso mosaganiza bwino.
Osamachepetsa kolemera.
-Osamaderera zinthu zomwe zingakuthandize.
Osamafunsa chinyezi kubafa.
-Mawuwa amanena za munthu amene akufunsa zinthu zoti aku-
zidziwa kale. Nanga ndi ndani amene angakhale pansi n’kuma-
funsa ngati kubafa kumakhala chinyezi kapena ayi?
196