Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Página 196
Miyambi ya Patsokwe
Nzeruzayekha adaphika nyemba zofumbwa.
-Kufunsa ena kumathandiza kuti tisapuse.
Nzeruzayekha anaviika nsima m’madzi.
-Kufunsa kumathandiza kuti tipewe kuchita zinthu zopanda
nzeru.
Nzimbe saidyera kutalika koma kuzuna.
-Maonekedwe amapusitsa. Tisamasankhe zinthu chifukwa cha
kukula kapena kuoneka bwino koma kulimba.
195