Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 184
Miyambi ya Patsokwe
Ngwazi nayonso imafa ndi mpeni umodzi.
-Ukakhala wamphamvu si bwino kumadzitama chifukwa um-
agwa ndi kanthu konyozeka.
Njala ikadza umaimangira kacheka.
-Kacheka ndi lamba kapena nsalu imene anthu amamanga
pamimba. Ukakhala pamavuto monga njala uyenera kuumanga
mtima kuti usaganize zakuba. Ngakhale zinthu zivute bwanji
ndi bwino kupitirizabe kuchita chilungamo.
Njala ikafika, ubale umatha.
-Anthu ambiri amakukonda ukakhala pabwino, zinthu zikavuta
amakuthawa.
Njala ili m’mano.
-Chakudya chingachepe, chimathandizabe kuti usafe.
Njala ndi kamtengo, kanagwetsa Undi.
-Njala imagwira aliyense ngakhale mfumu. Undi inali mfumu,
ndipo nayonso inagwa ndi kamtengo kameneka, njala.
Njala sailowetsa m’nkhokwe.
-Si bwino kuuza munthu yemwe akusowa chinachake kuti
atenge zimene akufuna chifukwa akhoza kumaliza zonse. Mun-
thu amene kwawo kuli njala sungamuuze kuti alowe munk-
hokwe, akhoza kukumalizirani chonse.
Njala ya mnzako ndi yako yomwe.
-Anzathu akakhala pamavuto monga matenda kapena imfa,
tiyenera kumawathandiza n’kumawamvera chisoni ngati zachi-
tikira ife.
Njala yapita pa mlimi.
-Nthawi zina pamakhala mavuto moti anthu amene timawada-
lira amakhalanso kuti sangatithandize. Zikatero timayenera ku-
chita zimene tikuona kuti zingatithandize.
183