Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 183
Miyambi ya Patsokwe
anthuanthu, ofooka sangazithe.
Ngati n’zotheka kuwapha ndi uchi, n’chifukwa chiyani ukufu-
na kuwapha ndi chiphe?
-Kumagwiritsa ntchito njira imene ukuona kuti ndi yabwino
kwambiri.
Ngati umakonda bwenzi lako, usamubwereke ndalama.
-Nthawi zambiri nkhani za ndalama zimachititsa kuti anthu asi-
yane. Tizisamala pa nkhani yobwereka ena ndalama. Ngati
munthu timagwirizana naye kwambiri, tingachite bwino
osamubwereka ndalama chifukwa akhoza kungotikhumud-
witsa.
Ngongole imakoma potenga, koma pobweza imawawa.
-Ukamatenga ngongole zimasangalatsa koma kuti ubweze pa-
makhala nkhani. Tiziganiza kaye tisanatenge ngongole.
Nguluwe inalira nsampha utaning’a.
-Nguluwe itagwidwa pansampha analimbana nawo mpaka
kutsala pang’ono kuduka. Koma m’malo molimbikira inatopa
ndipo inayamba kulira. Anthu atamva kulirako anabwera n’kud-
zaipha. Osamataya mtima msanga tikakhala pamavuto.
Nguluwe ya ana sinona.
-Nguluwe imene yabereka ana ambiri imakhala yoonda.
Chimodzimodzinso ndi munthu yemwe ali ndi ana ambiri
kapena amene amamudalira ambiri. Chifukwa ndalama zake
zimachuluka kopita, satukuka. Tizikhala ndi ana omwe
tingakwanitse kuwasamalira.
Nguwo yobwereka siilimba m’thupi.
-Nguwo ndi nsalu. Nsalu yobwereka simachedwa kugwa chifu-
kwa umakhala sunaizolowere. Tisamadalire za ena, tizipeza za-
thu.
182