Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 147
Miyambi ya Patsokwe
Mkazi wa mfumu akati mlomo tololo, wataya mudzi.
-Ngati mkazi wa mfumu ndi wolongolola, zinthu zimasokon-
ekera m’mudzi. Koma akakhala wofatsa zinthu zimayenda
bwino.
Mkazi wa mfumu asamati khutu petupetu.
-Mkazi wa mfumu asamakhale wamabodza chifukwa akhoza
kunamiza mwamuna wake n’kupasula mudzi. Mkazi wa
mtsogoleri ayenera kukhala wodziletsa.
Mkazi wabwino amaphika nsima yosazizira.
-Mkazi akamalandira bwino alendo, zimachititsa kuti mwamuna
wake akadzipita koyenda anthu adzamuphikire nsima. Zikatere
nsima anaphika mkazi wake ija imakhala ngati sinazizire.
Mkazi wophika msima yosazizira.
-Mawuwa amanenedwa potamanda mkazi amene amalandira
bwino alendo powaphikira chakudya chabwino. Mwamuna
wakenso amalandiridwa bwino akapita kwa anzake, m’mawu
ena nsima imene anaphika ija imakhala ngati ikutenthabe.
Mkhalamba msana, usiku ndi kamnyamata.
-Maonekedwe amapusitsa. Anthu ena amaoneka abwino pa-
maso, koma kuseri ali zilombo.
Mkoma akadadza.
-Pali anthu ena omwe amaonetsa makhalidwe abwino akakhala
kuchilendo, koma akakhazikika amayamba kuonetsa mawanga
awo enieni.
Mkuntho umodzi supha njoka.
-Pofuna kuchita zinthu pamafunika khama, osati kungochita ka-
modzi kokha. Mwachitsanzo, ngati ukufuna kulangiza munthu
kuti asiye khalidwe loipa, umayenera kuchita khama, apo ayi
njoka imene ili mwa iye singafe.
146